1 Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ace,
2 Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paskha ufika, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kupacikidwa pamtanda.
3 Pomwepo anasonkhana ansembe akuru, ndi akuru a anthu, ku bwalo la mkuru wa ansembe, dzina lace Kayafa;
4 nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi cinyengo, namuphe.
5 Koma ananena iwo, Pa dzuwa la cakudya iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.
6 Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate,