13 Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ici cimene mkaziyo anacitaci cidzakambidwanso cikumbukiro cace.
14 Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lace Yudase Isikariote, anamuka kwa ansembe akuru,
15 nati, Mufuna kundipatsa ciani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.
16 Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.
17 Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda cotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paskha, kuti mukadye?
18 Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena. Nthawi yanga yayandikirai ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.
19 Ndipo ophunzira anacita monga Yesu anawauza, nakonza Paskha.