26 Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ici ndi thupi langa.
27 Ndipo pamene anatenga cikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ici inu nonse,
28 pakuti ici ndici mwazi wanga wa pangano, wothiridwa cifukwa ca anthu ambiri ku kucotsa macimo.
29 Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso cipatso ici campesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa catsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga.
30 Ndipo pamene anayimba nyimbo, anaturuka kunka ku phiri la Azitona.
31 Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa cifukwa ca Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa,Ndidzakantha mbusa,Ndipo zidzabalalikaNkhosa za gulu.
32 Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.