30 Ndipo pamene anayimba nyimbo, anaturuka kunka ku phiri la Azitona.
31 Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa cifukwa ca Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa,Ndidzakantha mbusa,Ndipo zidzabalalikaNkhosa za gulu.
32 Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.
33 Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa cifukwa ca Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.
34 Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.
35 Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.
36 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo ku malo ochedwa Getsemane, nanena kwa ophunzira ace, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.