33 Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa cifukwa ca Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.
34 Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.
35 Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.
36 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo ku malo ochedwa Getsemane, nanena kwa ophunzira ace, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.
37 Ndipo anatenga Petro ndi ana awiria Zebedayo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi cisoni ndi kuthedwa nzeru.
38 Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uti wozingidwa ndi cisoni ca kufika naco kuimfa; khalani pano mucezere pamodzi ndi Ine.
39 Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yace pansi, napemphera, nati, Atate, ngati nkutheka, cikho ici cindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma lou.