39 Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yace pansi, napemphera, nati, Atate, ngati nkutheka, cikho ici cindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma lou.
40 Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? simukhoza kucezera ndi Ine mphindi imodzi?
41 Cezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uti wakufuna, koma thupi liri lolefuka.
42 Anamukanso kaciwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ici sicingandipitirire, koma ndimwere ici, kufuna kwanu kucitidwe.
43 Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo.
44 Ndipo anawasiyanso, napemphera kacitatu, nateronso mau omwewo.
45 Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa m'manja ocimwa.