17 Cifukwa cace pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wochedwa Kristu?
18 Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.
19 Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wace anatumiza mau kwa iye, kunena, Musacite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri cifukwa ca Iye.
20 Koma ansembe akuru anapangira anthu kuti apemphe Baraba, koma kuti aononge Yesu.
21 Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Baraba.
22 Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzacita ciani ndi Yesu, wochedwa Kristu?
23 Onse anati, Apacikidwe pamtanda. Ndipo iye anati, Cifukwa ninji? anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsa kopambana, Apacikidwe pamtanda.