21 Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Baraba.
22 Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzacita ciani ndi Yesu, wochedwa Kristu?
23 Onse anati, Apacikidwe pamtanda. Ndipo iye anati, Cifukwa ninji? anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsa kopambana, Apacikidwe pamtanda.
24 Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndiribe kucimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.
25 Ndipo anthu onse anabvomereza, ndi kuti, Mwazi wace uli pa ife ndi pa ana athu.
26 Pomwepo iye anamasulira iwo Baraba, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampacike pamtanda.
27 Pomwepo asilikari a kazembe anamuka naye Yesu ku bwalo la mirandu, nasonkhanitsa kwa iye khamu lao lonse.