11 Ndipo pameneiwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe akuru zonse zimene zinacitidwa.
12 Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akuru, anakhala upo, napatsa asilikariwo ndalama zambiri,
13 nati, Kazinenani, kuti ophunzira ace anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo.
14 Ndipo ngati ici cidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa.
15 Ndipo iwo analandira ndalamazo, nacita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.
16 Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangifa.
17 Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.