11 Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zace: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
12 couluzira cace ciri m'dzanja lace, ndipo adzayeretsa padwale pace; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wace m'ciruli, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.
13 Pamenepo Yesu anacokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.
14 Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?
15 Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa cilungamo conse motero. Pamenepo anamlola Iye.
16 Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anaturuka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;
17 ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.