2 nanena, Tembenukani mitima; cifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.
3 Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti,Mau a wopfuula m'cipululu,Konzani khwalala la Ambuye,Lungamitsani njira zace.
4 Ndipo Yohane yekhayo anali naco cobvala cace ca ubweya wangamila, ndi lamba lacikopa m'cuuno mwace; ndi cakudya cace cinali dzombe ndi uci wa kuthengo.
5 Pamenepo panamturukira iye ku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordano;
6 nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordano, alikuulula macimo ao.
7 Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wace, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
8 Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: