19 Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.
20 Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye.
21 Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedayo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.
22 Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.
23 Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumu, naciritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
24 Ndipo mbiri yace inabuka ku Suriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundu mitundu, ndi ogwidwa ndi mizimu yoipa, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawaciritsa.
25 Ndipo inamtsata mipingo mipingo ya anthu ocokera ku Galileya, ndi ku Dekapole ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordano.