5 Pamenepo mdierekezi anamuka naye ku mzinda woyera; namuika Iye pamwamba pa cimbudzi ca Kacisi,
6 nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti,Adzauza angelo ace za iwe,Ndipo pa manja ao adzakunyamulaiwe,Ungagunde konse phazi lako pamwala.
7 Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa,Usamuyese Ambuye Mulungu wako.
8 Pomwenso mdierekezi anamuka naye ku phiri lalitari, namuonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao;
9 nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.
10 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Coka Satana, pakuti kwalembedwa,Ambuye Mulungu wako udzamgwadira,Ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.
11 Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.