39 koma ndinena kwa inu, 11 Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako Lamanja, umtembenuzire linanso.
40 Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso copfunda cako.
41 Ndipo 12 amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.
42 Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye 13 wofuna kukukongola usampotolokere.
43 Munamva kuti kunanenedwa, 14 Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako:
44 koma Ine ndinena kwa inu, 15 Kondanani nao adani anu, ndi 16 kupempherera iwo akuzunza inu;
45 kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; cifukwa Iye amakwezera dzuwa lace pa oipa ndi pa abwino, namabvumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.