13 Lowani pa cipata copapatiza; cifukwa cipata ciri cacikuru, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa ico.
14 Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.
15 Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa.
16 Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?
17 Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa,
18 Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma.
19 Mtengo uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto.