21 pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze copfunda cace cokha ndidzacira.
22 Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, cikhulupiriro cako cakuciritsa. Ndipo mkaziyo anacira kuyambira nthawi yomweyo.
23 Ndipo Yesu polowa m'nyumba yace ya mkuruyo, ndi poona oyimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,
24 ananena, Turukani, pakuti kabuthuko sikanafa koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.
25 Koma pamene khamulo linaturutsidwa, Iye analowamo, nagwira dzanja lace; ndipo kabuthuko kadauka.
26 Ndipo mbiri yace imene inabuka m'dziko lonse limenelo.
27 Ndipo popita Yesu kucokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, opfuula ndi kuti, Muticitire ife cifundo, mwana wa Davide.