27 Ndipo popita Yesu kucokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, opfuula ndi kuti, Muticitire ife cifundo, mwana wa Davide.
28 Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kucita ici? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.
29 Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Cicitidwe kwa inu monga cikhulupiriro canu.
30 Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa Iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu ali yense.
31 Koma iwo anaturukamo, nabukitsa mbiri yace m'dziko lonselo.
32 Ndipo pamene iwo analikuturuka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi ciwanda.
33 Ndipo m'mene cinaturutsidwa ciwandaco, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sicinaoneke comweco mwa Israyeli.