29 Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Cicitidwe kwa inu monga cikhulupiriro canu.
30 Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa Iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu ali yense.
31 Koma iwo anaturukamo, nabukitsa mbiri yace m'dziko lonselo.
32 Ndipo pamene iwo analikuturuka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi ciwanda.
33 Ndipo m'mene cinaturutsidwa ciwandaco, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sicinaoneke comweco mwa Israyeli.
34 Koma Afarisi analinkunena, Aturutsa ziwanda ndi mphamvu zace za mfumu ya ziwanda.
35 Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, naciritsa nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.