9 Ndipo Yesu popita, kucokera kumeneko, anaona munthu, dzina lace Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
10 Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pacakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ocimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace.
11 Ndipo Afarisi, pakuona ici, ananena kwa ophunzira ace, Cifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ocimwa?
12 Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala.
13 Koma mukani muphunzire nciani ici:Ndifuna cifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa.
14 Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ace a Yohane, nati, Cifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawiri kawiri, koma ophunzira anu sasala?
15 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? koma adzafika masiku, pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.