28 Koma muceukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lace, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwace kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero;
29 kuti maso anu atsegukire nyumba yino usiku ndi usana, kumalo kumene munanenako, Dzina langa lidzakhala komweko; kuti mumvere pemphero limene adzapemphera kapolo wanu lolunjika kumalo kuno.
30 Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisrayeli, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.
31 Ngati munthu akacimwira mnzace, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba yino;
32 mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo citani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera cimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga cilungamo cace.
33 Ndipo anthu anu Aisrayeli akawakantha adani ao cifukwa ca kucimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, lodi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;
34 pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira cimo la anthu anu Aisrayeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.