30 Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisrayeli, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.
31 Ngati munthu akacimwira mnzace, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba yino;
32 mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo citani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera cimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga cilungamo cace.
33 Ndipo anthu anu Aisrayeli akawakantha adani ao cifukwa ca kucimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, lodi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;
34 pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira cimo la anthu anu Aisrayeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.
35 Pamene kumwamba kwatsekeka, ndipo kulibe mvula cifukwa ca kucimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;
36 pamenepo mverani Inu m'Mwamba, ndi kukhululukira cimo la akapolo anu, ndi la, anthu anu Aisrayeli; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula pa: dziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale colowa cao.