1 Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-damimu.
2 Ndipo Sauli ndi anthu a Israyeli anasonkhana, namanga zithando pa cigwa ca Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.
3 Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisrayeli anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali cigwa.
4 Ndipo ku zithando za Afilisti kunaturuka ciwinda, dzina lace Goliate wa ku Gati, kutalika kwace ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi cikhato.
5 Ndipo anali ndi cisoti camkuwa pamutu pace, nabvala maraya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa,
6 nakuta msongolo wace ndi cobvala camkuwa, ndiponso pacikota pace panali nthungo yamkuwa.