1 Motero Davide anacoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ace ndi banja lonse la atate wace anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.
2 Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.
3 Ndipo Davide anacoka kumeneko kunka ku Mizipa wa ku Moabu; nati kwa mfumu ya Moabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga aturuke nakhale nanu, kufikira ndidziwa cimene Mulungu adzandidtira.
4 Ndipo anawatenga kumka nao pamaso pa mfumu ya Moabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo.
5 Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; cokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anacokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.
6 Pakumva Sauli kuti anadziwika Davide, ndi anthu ace akukhala naye, Sauti analikukhala m'Gibeya, patsinde pa mtengo wa kumsanje, m'dzanja lace munali mkondo wace, ndi anyamata ace onse anaimirira pali iye.
7 Ndipo Sauli anati kwa anyamata ace akuima comzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Jese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yamphesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;
8 kuti inu nonse munapangana dwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Jese, ndipo palibe wilia wa inu wakundidtira cifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?
9 Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Sauli, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Jeseyo alikufika ku Nobi, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubu.
10 Ndipo iye anamfunsira kwa Yehova, nampatsa cakudya, nampatsanso lupanga la Gotiate Mfilistiyo.
11 Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubu, ndi banja lonse la atate wace, ansembe a ku Nobi; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.
12 Ndipo Sauli anati, Imva tsopano iwe mwana wa Ahitubu. Nayankha iye, Ndine, mbuye wanga.
13 Ndipo Sauli anati kwa iye, Munapangana dwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Jese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?
14 Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu?
15 Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wace kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.
16 Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako.
17 Mfumu niuza asilikari akuima comzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; cifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululira. Koma anayamata a mfumu sanafuna kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.
18 Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akubvala efodi wabafuta.
19 Ndipo anakantha Nobi ndiwo mudzi wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi aburu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.
20 Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubu, dzina lace ndiye Abyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide.
21 Ndipo Abyatara anadziwitsa Davide kuti Sauli anapha ansembe a Yehova.
22 Ndipo Davide anati kwa Abyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Sauli; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako.
23 Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika.