1 Samueli 11 BL92

Sauli alanditsa Yabezi Gileadi m'manja mwa Aamoni

1 Pamenepo Nahasi M-amoni anakwera, namanga Yabezi Gileadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabezi anati kwa Nahasi, Mupangane cipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.

2 Ndipo Nahasi Mamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisrayeli onse.

3 Ndipo akuru a ku Yabezi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israyeli; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzaturukira kwa inu.

4 Tsono mithengayo inafika ku Gibeya kwa Sauli, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.

5 Ndipo, onani, Sauli anacokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Sauli, Coliritsa anthu misozi nciani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabezi.

6 Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Sauli mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wace unayaka kwambiri.

7 Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthuli nthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israyeli, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Sauli ndi pa Samueli, adzatero nazo ng'ombe zace. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, naturuka ngati munthu mmodzi.

8 Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israyeli anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu.

9 Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabezi Gileadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona cipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabezi; nakondwara iwowa.

10 Cifukwa cace anthu a ku Yabezi anati, Mawa tidzaturukira kwa inu, ndipo mudzaticitira cokomera inu.

11 Ndipo m'mawa mwace Sauli anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo m'ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.

12 Ndipo anthu anati kwa Samueli, Ndani iye amene anati, Kodi Sauli adzatiweruza ife? tengani anthuwo kuti tiwaphe.

13 Koma Sauli anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anacita cipulumutso m'lsrayeli.

14 Ndipo Samueli ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko.

15 Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Sauli mfumu pamaso pa Yehova m'Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Sauli ndi anthu onse a Israyeli anakondwera kwakukuru.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31