1 Samueli 21 BL92

Davide athawira kwa wansembe Ahimeleki ku Nobi

1 Ndipo Davide anafika ku Nobi kwa! Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?

2 Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira nchito, ninena nane, Asadziwe munthu ali yense kanthu za nchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.

3 Cifukwa cace tsono muli ndi ciani? mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena ciri conse muli naco.

4 Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndiribe mkate wacabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.

5 Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; cicokere ine, zotengera za anayamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wacabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?

6 Comweco wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adaucotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anacotsa winawo.

7 Tsono munthu wina wa anyamata a Sauli anali komweko, tsiku lija, anacedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lace ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Sauli.

8 Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? cifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mrandu wa mfumu ukuti ndifulumire.

9 Nati wansembeyo, Lupanga la Goliate Mfilisti munamuphayo m'cigwa ca Ela, onani-liripo lokulunga m'nsaru, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina, Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni.

Davide athawira kwa Akisi

10 Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo cifukwa ca kuopa Sauli, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati.

11 Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti,Sauli anapha zikwi zace,Koma Davide zikwi zace zankhani?

12 Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwace, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.

13 Nasanduliza makhalidwe ace pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za cipata, nakhetsa dobvu lace pa ndebvu yace.

14 Tsono Akisi ananena ndi anyamata ace, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine cifukwa ninji?

15 Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m'nyumba mwanga?

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31