1 Samueli 25 BL92

Amwalira Samueli

1 Ndipo Samueli anamwalira; ndi Aisrayeli onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ace, namuika m'nyumba yace ku Rama. Davide nanyamuka, natsikira ku cipululu ca Parana.

Za Davide, Nabala ndi Abigayeli

2 Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wace anali ku Karimeli; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi cikwi cimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zace ku Karimeli.

3 Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wace ndiye Abigayeli; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa macitidwe ace; ndipo iye anali wa banja la Kalebi.

4 Ndipo Davide anamva kucipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zace.

5 Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo, Mukwere ku Karimeli, mumuke kwa Nabala ndi kundilankhulira iye;

6 ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.

7 Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawacititsa manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimeli.

8 Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; cifukwa cace muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tirikufika tsiku labwino; mupatse ciri conse muli naco m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.

9 Ndipo pakufika anyamata a Davide, analankhula ndi Nabala monga mau aja onse m'dzina la Davide, naleka.

10 Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? ndi mwana walese ndani? Makono ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.

11 Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira?

12 Comweco anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa.

13 Ndipo Davide anati kwa anthu ace, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lace. Namangirira munthu yense lupanga lace; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lace; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.

14 Koma mnyamata wina anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akucokera kucipululu kulankhula mbuye wathu; koma iye anawakalipira.

15 Koma anthu aja anaticitira zabwino ndithu, sanaticititsa manyazi, ndi panalibe kanthu kadatisowa, nthawi zonse tinali kuyenderana nao kubusa kuja;

16 iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo.

17 Cifukwa cace tsono mudziwe ndi kulingalira cimene mudzacita; popeza anatsimikiza mtima kucitira coipa mbuye wathu, ndi nyumba yace yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.

18 Pomwepo Abigayeli anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoocaoca, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi ncinci za mphesa zouma zana limodzi, ndi ncinci za nkhuyu mazana awiri, naziika pa aburu.

19 Nati kwa anyamataace, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuvo mwanu. Koma sanauza mwamuna wace Nabala.

20 Ndipo kudatero pakuberekeka iye pa buru wace, natsikira pa malo obisika a m'phirilo, onani, Davide ndi anthu ace analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao.

21 Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga cabe zace zonse za kaja kanali nazo m'cipululu, sikadasowa kanthu ka zace zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

22 Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo.

23 Ndipo Abigayeli pakuona Davide, anafulumira kutsika pa bum, nagwa pamaso pa Davide nkhope yace pansi, namgwadira,

24 Ndipo atagwadira pa mapazi ace anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale ucimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.

25 Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; cifukwa monga dzina lace momwemo iye; dzina lace ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaona anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza.

26 Cifukwa cace tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera cilango ndi dzanja la inu nokha, cifukwa cace adani anu, ndi iwo akufuna kucitira mbuye wanga coipa, akhale ngati Nabala.

27 Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.

28 Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka coipa masiku anu onse.

29 Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga coturuka m'coponyera mwala.

30 Ndipo kudzali, pamene Yehova anacitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israyeli;

31 mudzakhala opanda cakudodoma naco, kapena cakusauka naco mtima wa mbuye wanga, cakuti munakhetsa mwazi wopanda cifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera cilango; ndipo Yehova akadzacitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukile mdzakazi wanu.

32 Ndipa Davide anati kwa Abigayeli, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anakutumiza lero kudzandicingamira ine;

33 ndipo, kudalitsike kucenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera cilango ndi dzanja la ine ndekha.

34 Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundicingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutaca kanthu konse, ngakhale mwana wamwamunammodzi.

35 Comweco Davide analandira m'dzanja lace zimene iye anamtengera; nanena naye, Ukwere kwanu mumtendere; ona, ndamvera mau ako, ndabvomereza nkhope yako.

36 Ndipo Abigayeli anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwace, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwace, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuza kanthu konse, kufikira kutaca.

37 Tsono m'mawa vinyo atamcokera Nabala, mkazi wace anamuuza zimenezi; ndipo mtima wace unamyuka m'kati mwace, iye nasanduka ngati mwala.

38 Ndipo kunali, atapita masiku khumi, Yehova anamkantha Nabala, nafa.

39 Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mrandu wa mtonzo wanga wocokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wace pa coipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala coipa cace. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigayeli, zakuti amtengere akhale mkazi wace.

40 Ndipo anyamata a Davide pakufika kwa Abigayeli ku Karimeli, analankhula naye, nati, Davide anatitumiza kwa inu, kukutengani, mukhale mkazi wace.

41 Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yace pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.

42 Ndipo Abigayeli anafulumira nanyamuka, nakwera pa bum, pamodzi ndi anamwali ace asanu akumtsata; natsatira mithenga ya Davide, nakhala mkazi wace.

43 Davide anatenganso Ahinoamu wa ku Yezreeli, ndipo onse awiri anakhala akazi ace.

44 Pakuti Sauli anapatsa Mikala, mwana wace, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Loisi, wa ku Galimu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31