1 Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisrayeli. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzaturuka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako.
2 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe cimene mnyamata wanu adzacita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Cifukwa cace ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.
3 M'menemo Samueli ndipo atafa, ndipo Aisrayeli onse atalira maliro ace, namuika m'Rama, m'mudzi mwao. Ndipo Sauli anacotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse.
4 Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Sauli anasonkhanitsa Aisrayeli onse, namanga iwo ku Giliboa.
5 Ndipo pamene Sauli anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wace unanjenjemera kwakukuru.
6 Ndipo pamene Sauli anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankha ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.
7 Tsono Sauli anati kwa anyamata ace, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ace anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta.
8 Ndipo Sauli anadzizimbaitsa nabvala zobvala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire ali yense ndidzakuchulira dzina lace.
9 Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa cimene anacita Sauli, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; cifukwa ninji tsono mulikuchera moyo wanga msampha, kundifetsa.
10 Ndipo Sauli anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe cilango cidzakugwera cifukwa ca cinthu ici.
11 Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samueli.
12 Ndipo mkaziyo pakuona Samueli, anapfuula ndi mau akuru; ndi mkaziyo analankhula ndi Sauli, nati, Munandinyengeranji? popeza inu ndinu Sauli.
13 Ndipo mfumuvo inanena naye, Usaope, kodi ulikuona ciani? Mkaziyo nanena ndi Sauli, Ndirikuona milungu irikukwera kuturuka m'kati mwa dziko.
14 Ndipo ananena naye, Makhalidwe ace ndi otani? nati iye, Nkhalamba irikukwera yobvala mwinjiro. Pamenepo Sauli anazindikira kuti ndi Samueli, naweramitsa nkhope yace pansi, namgwadira.
15 Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Wandibvutiranji kundikweretsa kuno? Sauli nayankha, Ndirikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandicokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; cifukwa cace ndakuitanani, kuti mundidziwitse cimene ndiyenera kucita.
16 Ndip'o Samueli ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakucokera, nasandulika mdani wako?
17 Ndipo Yehova yekha wacita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuucotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.
18 Cifukwa sunamvera mau a Yehova, ndi kukwaniritsa mkwiyo wace woopsa pa Ameleki, cifukwa cace Yehova wakucitira cinthu ici lero.
19 Ndiponso Yehova adzapereka Israyeli pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisrayeli m'dzanja la Afilisti.
20 Pomwepo Sauli anagwa pansi tantha, naopa kwakukuru, cifukwa ca mau a Samueli; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wace wonse anakhala osadya kanthu.
21 Ndipo mkaziyo anafika kwa Sauli, naona kuti ali wobvutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine.
22 Cifukwa cace tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.
23 Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ace, pamodzi ndi mkaziyo anamkangamiza; iyenamvera mau ao. Comweco anauka pansi, nakhala pakama.
24 Ndipo mkaziyo anali ndi mwana wa ng'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda cotupitsa;
25 nabwera nazo kwa Sauli ndi kwa anyamata ace; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nacoka usiku womwewo.