1 Samueli 4 BL92

Afilisti akantha Aisrayeli

1 Ndipo mau a Samueli anafikira kwa Aisrayeli onse. Ndipo Aisrayeli anaturuka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga m'Afeki.

2 Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisrayeli; ndipo pokomana nkhondo Aisrayeli anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.

Likasa lilandidwa, Hofeni ndi Pinehasi aphedwa

3 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akuru a Israyeli anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la cipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.

4 Cifukwa cace anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la cipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Pinehasi anali komweko ndi likasa la cipangano la Yehova.

5 Pakufika likasalo la cipangano la Yehova kuzithando, Aisrayeli onse anapfuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linacita cibvomezi.

6 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kupfuula kwao, anati, Phokoso ili la kupfuula kwakukuru ku zithando za Aisrayeli litani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidzafika ku zithandozo.

7 Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! popeza kale lonse panalibe cinthu cotere.

8 Tsoka kwa ife! adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aaigupto ndi masautso onse m'cipululu ndi yomweyi.

9 Limbikani, ndipo mucite camuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Citani camuna nimuponyane nao.

10 Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisrayeli; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wace; ndipo kunali kuwapha kwakukuru; popeza anafako Aisrayeli zikwi makumi atatu a oyenda pansi.

11 Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinehasi, anaphedwa.

12 Ndipo munthu wa pfuko la Benjamini anathamanga kucokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace.

Imfa ya Eli

13 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wace unanthunthumira cifukwa ca likasa la Mulungu, Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira.

14 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.

15 Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ace anangokhala tong'o osapenya,

16 Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndacokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, a Nkhondoyo idatani, mwana wanga?

17 Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, lsrayeli anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukuru kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Pinehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandiwa.

18 Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa cambuyo pa mpando wace pam bali pa cipata, ndi khosi lace linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkuru thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israyeli zaka makumi anai.

19 Ndipo mpongozi wace, mkazi wa Pinehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yace yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wace, ndi mwamuna wace anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kucira kwace kwamdzera.

20 Ndipo pamene adati amwalire, anthu akazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankha, kapena kusamalira.

21 Ndipo iye anamucha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wacoka kwa Israyeli; cifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi cifukwa ca mpongozi wace ndi mwamuna wace.

22 Ndipo iye anati, Ulemerero wacoka kwa Israyeli; cifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31