1 Samueli 12 BL92

Samueli adzinenera kwa anthu

1 Ndipo Samueli anauza Aisrayeli onse, kuti, Onani dani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu.

2 Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga amuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.

3 Ndikalipo ine; citani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wace; ndinalanda ng'ombe ya yani? kapena ndinalanda buru wa yani? ndinanyenga yani? ndinasautsa yani? ndinalandira m'manja mwa yani cokometsera mlandu kutseka naco maso anga? ngati ndinatero ndidzacibwezera kwa inu.

4 Ndipo iwo anati, Simunatinyenga, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina ali yense.

5 Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wace ali mboni lero kuti simunapeza kanthu m'dzanja langa, Nati iwo, iye ali mboni.

6 Ndipo Samueli ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, naturutsanso makolo anu m'dziko la Aigupto,

7 Cifukwa cace tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova za nchito zonse zolungama za Yehova, anakucitirani inu ndi makolo anu.

8 Pamene Yakobo anafika ku Aigupto, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anaturutsa makolo anu m'Aigupto, nawakhalitsa pamalo pano,

9 Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Moabu, iwo naponyana nao.

10 Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinacimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.

11 Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Bedani, ndi Yefita, ndi Samueli, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.

12 Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu.

13 Cifukwa cace siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.

14 Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ace, ndi kusakana lamulo lace la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, cabwino.

15 Koma mukapanda kumvera mau a Yehova, ndi kupikisana ndi lamulo la Yehova, dzanja la Yehova lidzatsutsana nanu, monga linatsutsana ndi makolo anu.

16 Cifukwa cace tsono, imani pano, muone cinthu ici cacikuru Yehova adzacicita pamaso panu.

17 Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atomize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti coipa canu munacicita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, ncacikuru.

18 Momwemo Samueli anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.

19 Ndipo anthu onse ananena ndi Samueli, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza coipa ici, cakuti tinadzipemphera mfumu.

20 Ndipo Samueli ananena kwa anthuwo, Musaope; munacitadi coipa ici conse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;

21 musapambukire inu kutsata zinthu zacabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza ziri zopanda pace.

22 Pakuti Yehova sadzasiya anthu ace cifukwa ca dzina lace lalikuru; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a iye yekha.

23 Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kucimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.

24 Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuruzo iye anakucitirani.

25 Koma mukaumirirabe kucita coipa, mudzaonongeka, inu ndi mfumu yanu yomwe.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31