1 Samueli 3 BL92

Masomphenya a Samueli

1 Ndipo mwanayo Samueli anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzi kamodzi; masomphenya sanaoneka-oneka.

2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwace (maso ace anayamba cizirezire osatha kupenya bwino);

3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samueli nagona m'Kacisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.

4 Pamenepo Yehova anaitana Samueli; ndipo iye anayankha kuti, Ndiri pano.

5 Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitana, kagone. Napita iye, nagona,

6 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samueli. Ndipo Samueli anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone.

7 Koma Samueli sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.

8 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samueli nthawi yacitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.

9 Cifukwa cace Eli anati kwa Samueli, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukabvomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Comweco Samueli anakagona m'malo mwace.

10 Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samueli, Samueli. Pompo Samueli anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.

11 Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Taona, ndidzacita mwa Israyeli coliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakucimva.

12 Tsiku lija udidzamcitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lace, kuciyamba ndi kucitsiriza.

13 Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yace kosatha cifukwa ca zoipa anazidziwa, popeza ana ace anadzitengera temberero, koma iye sanawaletsa.

14 Cifukwa cace ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.

Samueli aulula kwa Eli

15 Ndipo Samueli anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samueli anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.

16 Pamenepo Eli anaitana Samueli, nati, Mwana wanga, Samueli. Nati iye, Ndine.

17 Ndipo anati, Anakuuza cinthu canji? Usandibisire ine. Mulungu akulangendi kuonjezapo, ngati undibisira cimodzi ca zonse zija adanena nawe.

18 Ndipo Samueli anamuuza zonse, sanambisira kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; acite comkomera pamaso pace.

19 Ndipo Samueli anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ace amodzi apite pacabe.

20 Ndipo Aisrayeli onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samueli anakhazikika akhale mneneri wa Yehova.

21 Ndipo Yehova anaonekanso m'Silo, pakuti Yehova anadziulula kwa Samueli ku Silo, mwa mau a Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31