1 Ndipo Sauli analankhula kwa Jonatani mwana wace, ndi anyamata ace onse kuti amuphe Davide.
2 Koma Jonatani mwana wa Sauli anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Jonatani anauza Davide, nati, Sauli atate wanga alikufuna kukupha; cifukwa cace tsono ucenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale;
3 ndipo ine ndidzaturuka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa.
4 Ndipo Jonatani analankhula ndi atate wace mobvomereza Davide, nanena naye, Mfumu asacimwire mnyamata wace Davide; cifukwa iyeyo sanacimwira inu, ndipo nchito zace anakucitirani zinali zabwino ndithu;
5 popeza iye anataya moyo wace nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anacitira Aisrayeli onse cipulumutso cacikuru, inu munaciona, nimnnakondwera; tsono mudzacimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda cifukwa?
6 Ndipo Sauli anamvera mau a Jonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye.
7 Pamenepo Jonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Jonatani anafika naye Davide kwa Sauli, iye nakhalanso pamaso pace monga kale.
8 Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anaturuka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe akuru, ndipo iwo anamthawa iye.
9 Ndipo mzimu woipa wocokera kwa Yehova unali pa Sauli, pakukhala iye m'nyumba mwace, ndi mkondo wace m'dzanja lace; ndipo Davide anayimba ndi dzanja lace.
10 Ndipo Sauli anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kucoka pamaso pa Sauli; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.
11 Ndipo Sauli anatumiza mithenga ku nyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa.
12 Comweco Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.
13 Ndipo Mikala anatenga cifanizo naciika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwace, nacipfunda zopfunda.
14 Ndipo pamene Sauli anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, iye alikudwala.
15 Ndipo Sauli anatumiza mithengayo kuti ikaone Davide, nati, Mumtengere iye pa kama wace, kuti ndidzamuphe.
16 Ndipopakulowamithengayo, onani, pakama pali cifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwace.
17 Nati Sauli kwa Mikala, Wandinyengeranii comweci, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Sauli, iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.
18 Comweco anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samueli: ku Rama, namuuza zonse Sauli anamcitira. Ndipo iye ndi Samueli anakhala ku Nayoti.
19 Ndipo wina anauza Sauli, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti m'Rama.
20 Ndipo Sauli anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samueli mkuru wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera-mithenga ya Sauli, ninenera iyonso.
21 Ndipo pamene anauza Sauli, iye anatumiza mithenga yina; koma iyonso inanenera. Ndipo Sauli anatumiza mithenga kacitatu, nayonso inanenera.
22 Pamenepo iyenso anamuka ku Rama, nafika ku citsime cacikuru ciri ku Seku, nafunsa Dati, Samueli ndi Davide ali kuti? Ndipo wina anati, Taonani, ali ku Nayoti m'Rama.
23 Ndipo anapita komweko ku Nayoti m'Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti m'Rama.
24 Ndiponso anabvula zobvala zace, naneneranso pamaso pa Samueli nagona wamarisece usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Cifukwa cace amati, Kodi Saulinso ali pakati pa aneneri?