1 Samueli 26 BL92

Davide alekanso Sauli osamupha

1 Ndipo Azifi anafika kwa Sauli ku Gibeya, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hagila, kupenya kucipululu!

2 Ndipo Sauli ananyamuka, natsikira ku cipululu ca Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israyeli osankhika, kukafuna Davide m'cipululu ca Zifi.

3 Sauli namanga zithando m'phiri la Hagila kupenya kucipululu kunjira, Koma Davide anakhala kucipululu, naona kuti Sauli alikumfuna kucipululu komweko.

4 Cifukwa cace Davide anatumiza ozonda, nazindikira kuti Sauli anabwera ndithu,

5 Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo pala Sauli anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Sauli, ndi Abineri mwana wa Neri kazembe wa khamu lace; ndipo Sauli anagona pakati pa linga la magareta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pace.

6 Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Mhiti, ndi Abisai mwana wa Zeruya, mbale wace wa Yoabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Sauli? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.

7 Comweco Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Sauli anagona tulo m'kati mwa linga la magareta, ndi mkondo wace wozika kumutu kwace; ndi Abineri ndi anthuwo anagona pomzinga iye.

8 Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.

9 Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lace pa wodzozedwa wa Mulungu, ndi kukhala wosacimwa?

10 Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yace lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.

11 Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwace, ndi cikho ca madzi, ndipo tiyeni, timuke.

12 Comweco Davide anatenga mkondowo, ndi cikho ca madzi ku mutu wa Sauli nacoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anati m'tulo; popeza tulo tatikuru tocokera kwa Yehova tinawagwira onse.

13 Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba pa phiri; pakati pao panati danga lalikuru;

14 ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abineri mwana wa Neri, nati, Suyankha kodi Abineri? Tsono Abineri anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?

15 Davide nati kwa Abineri, Si ndiwe mwamuna weni weni kodi? ndani mwa Aisrayeli afanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.

16 Ici unacicita siciri cabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, cifukwa simunadikira mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi cikho ca madzi zinali kumutu kwace ziri kuti?

17 Ndipo Sauli anazindikira mau ace a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.

18 Nati iye, Cifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wace? pakuti ndacitanji? kapena m'dzanja langa muli coipa cotani?

19 Cifukwa cace mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wace. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire copereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipitikitsa lero kuti ndisalandireko colowa ca Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu yina.

20 Cifukwa cace tsono, mwazi wanga usagwe pansi kutati ndi Yehova; pakuti mfumu ya Israyeli yaturuka kudzafuna nsabwe, monga munthu wosaka nkhwali pamapiri.

21 Pamenepo Sauli anati, Ndinacimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakucitiranso coipa, popeza moyo wanga unati wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukuru.

22 Davide nayankha, nati, Tapenyani lmkondo wa mfumu Abwere mnyamata wina kuutenga.

23 Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense cilungamo cace ndi cikhulupiriko cace, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalola kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova,

24 Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo iye andipulumutse ku masautso onse.

25 Pomwepo Sauli anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzacita ndithu camphamvu, nudzapambana. Comweco Davide anamuka, ndipo Sauli anabwera kwao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31