1 Samueli 10 BL92

Samueli; adzoza Sauli akhale mfumu ya Israyeli

1 Pamenepo Samueli anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pace, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozani ndi Mulungu kodi, mukhale mfumu ya pa colowa cace?

2 M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Aburu aja munakafuna, anapezedwa; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira aburuwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzacita ciani, cifukwa ca mwana wanga?

3 Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Beteli, wina wonyamula ana a mbuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.

4 Iwowa adzakulankhulani, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao.

5 Ndipo m'tsogolo mwace mudzafika ku phiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi cisakasa, ndi lingaka, ndi toliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;

6 ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.

7 Ndipo zitakufikirani zizindikilo izi mudzacita monga mudzaona pocita, pakuti Mulungu ali nanu.

8 Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani cimene mudzacita.

9 Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samueli, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikilo zija zonse zinacitika tsiku lija.

Sauli pakati pa aneneri

10 Ndipo pamene anafika kucitunda kuja, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao,

11 Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ici cakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzace, Ici nciani cinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulinso ali mwa aneneri?

12 Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Cifukwa cace mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulinso ali mwa aneneri?

13 Ndipo pamene adatha kunenera anafika kumsanjeko.

14 Ndipo mbale wa atate wace wa Sauli ananena kwa iye ndi mnyamata wace, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna aburuwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samueli.

15 Ndipo mbale wa atate wa Sauli anati, Undiuze cimene Samueli analankhula nawe.

16 Ndipo Sauli anati kwa mbale wa atate wace, Anatiuza momveka kuti aburuwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitsa mau aja Samueli ananena zaufumuwo.

Anthu abvomereza Sauli akhale mfumu yao

17 Ndipo Samueli anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;

18 nanena ndi ana a Israyeli, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli kuti, Ine ndinaturutsa Israyeli m'Aigupto, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aaigupto, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani;

19 koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Cifukwa cace tsono mudzionetse pamaso pa Mulungu mafuko mafuko, ndi magulu magulu.

20 Comweco Samueli anayandikizitsa mafuko onse a Israyeli, ndipo pfuko la Benjamini linasankhidwa.

21 Nayandikizitsa pfuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Sauli mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.

22 Cifukwa cace anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.

23 Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa anthu onse anamlekeza m'cifuwa.

24 Ndipo Samueli ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anapfuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.

25 Pamenepo Samueli anafotokozera anthu macitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samueli anauza anthu onse amuke, yense ku nyumba yace,

26 Ndi Sauli yemwe anamuka ku nyumba yace ku Gibeya; ndipo am'khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao.

27 Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala cete.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31