1 Samueli 14 BL92

Jonatani agonjetsa Afilisti

1 Ndipo kunali tsiku lina kuti Jonatani mwana wa Sauli ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauza atate wace.

2 Ndipo Sauli analikukhala m'matsekerezo a Gibeya patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migroni; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;

3 ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wace wa Ikabodi, mwana wa Pinehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wobvala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwa kuti Jonatani wacoka.

4 Ndipo pakati pa mipata imene Jonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali yina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzace; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzace ndilo Sene.

5 Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzace kumwera pandunji pa Geba.

6 Ndipo Jonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zace, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira nchito; pakuti palibe comletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.

7 Ndipo wonyamula zida zace ananena naye, Citani zonse ziri mumtima mwanu; palukani, onani ndiri pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.

8 Ndipo Jonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziu lula kwa iwo.

9 Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo.

10 Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ici cidzatikhalira cizindikilo.

11 Ndipo onse awiri anadziulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikuturuka m'mauna m'mene anabisala.

12 Ndipo a ku kabomawo anayankha Jonatani ndi wonyamula zida zace, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Jonatani anauza wonyamula zida zace, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israyeli.

13 Ndipo Jonatani anakwera cokwawa, ndi wonyamula zida zace anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Jonatani, ndi wonyamula zida zace anawapha pambuyo pace.

14 Kuwapha koyambako, Jonatani ndi wonyamula zida zace, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng'ombe ziwiri tsiku limodzi.

15 Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; comweco kunali kunthunthumira kwakukuru koposa,

16 Ndipo ozonda a Sauli ku Gibeya wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.

Sauli alumbirira anthu

17 Pamenepo Sauli ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anaticokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Jonatani ndi wonyamula zida zace panalibe.

18 Ndipo Sauli ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israyeli.

19 Ndipo kunali m'mene Sauli anali cilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m'cigono ca Afilisti linacitikabe, nilikula; ndipo Sauli ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako.

20 Ndipo Sauli ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, naturukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzace ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukuru.

21 Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anaturuka m'dziko lozungulira kukaiowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisrayeli amene anali ndi Sauli ndi Jonatani.

22 Anateronso Aisrayeli onse akubisala m'phiri la Efraimu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapitikitsa kolimba kunkhondoko.

23 Comweco Yehova anapulumutsa Israyeli tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.

24 Ndipo Aisrayeli anasauka tsiku lija; pakuti Sauli anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere cilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.

25 Ndipo anthu onsewo analowa munkhalango, panali uci pansi.

26 Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uci anacuruka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lace pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.

27 Koma Jonatani sanamva m'mene atate wace analumbirira anthu; cifukwa cace iye ana tam balitsa ndodo ya m'dzanja lace, naitosa m'cisa ca uci, naika dzanja lace pakamwa pace; ndipo m'maso mwace munayera.

28 Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero cakudya. Ndipo anthuwo analema.

29 Ndipo Jonatani anati, Atate wanga wabvuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, cifukwa ndinalawako pang'ono uciwu.

30 Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? popeza tsopano palibe kuwapha kwakukuru kwa Afilisti.

31 Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ajaloni, ndipo anthu anafoka kwambiri.

32 Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi ana a ng'ombe, naziphera pansi; anthu nazidya ziri ndi mwazi wao.

33 Pamenepo anauza Sauli, kuti, Onani anthu alikucimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munacita konyenga; kunkhunizani mwala waukuru kwa ine lero.

34 Ndipo Sauli anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yace, ndi munthu yense ndi nkhosa yace, aziphe pano, ndi kuzidya, osacimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yace, usiku uja naziphera pomwepo.

35 Ndipo Sauli anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova.

Jonatani atsutsidwa ale

36 Ndipo Sauli anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Citani ciri conse cikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno.

37 Ndipo Sauli anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja la Israyeli kodi? Koma iye sanamyankha tsiku lomweli.

38 Ndipo Sauli anati, Musendere kuno, inu nonse akuru a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli coipa ici lero.

39 Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israyeli, cingakhale ciri m'mwana wanga Jonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.

40 Ndipo iye ananena ndi Aisrayeli onse, Inu mukhale mbali yina, ndipo me ndi Jonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Sauli, Citani cimene cikukomerani.

41 Cifukwa cace Sauli ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israyeli, muonetse coonadi. Ndipo maere anagwera Sauli ndi Jonatani; koma anthuwo anapulumuka.

42 Ndipo Sauli anati, Mucite maere pakati pa ine ndi Jonatani mwana wanga. Ndipo anagwera Jonatani.

43 Pamenepo Sauli ananena ndi Jonatani, Undiuze cimene unacita. Ndipo Jonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uci pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.

44 Pamenepo Sauli anati, Mulungu andilange, naoniezereko, pakuti udzafa ndithu, Jonatani.

Anthu alanditsa Jonatani

45 Ndipo anthuwo ananena ndi Sauli, Kodi Jonatani adzafa, amene anacititsa cipulumutso cacikuru ici m'Israyeli? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wace lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Comweco anthuwo anapulumutsa Jonatani kuti angafe. Ndipo Sauli analeka kuwapitikitsa Afilistiwo;

46 ndi Afilistiwo anamuka ku malo a iwo okha.

47 Ndipo pamene Sauli atakhazikitsa ufumu wa pa Israyeli, iye anaponyana ndi adani ace onse pozungulira ponse, ndi Moabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo pali ponse anapotolokerapo, anawalanga.

48 Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleki, napulumutsa Aisrayeli m'manja a akuwawawanya.

49 Ndipo ana a Sauli ndiwo Jonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana akazi ace awm ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabu, ndi dzina la mng'ono wace ndiye Mikala;

50 ndi dzina la mkazi wa Sauli ndi Ahinamu mwana wa Ahimazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lace ndiye Abineri mwana wa Neri, mbale wace wa atate wa Sauli.

51 Ndipo atate wa Sauli ndiye Kisi; ndipo Neri atate wa Abineri ndiye mwana wa Abiyeli.

52 Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Sauli; ndipo Sauli pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31