1 Samueli 20 BL92

Pangano pakati pa Davide ndi Jonatani

1 Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Jonatani, Ndacitanji ine? kuipa kwanga kuli kotani? ndi chimo langa la pamaso pa atate wanu ndi ciani, kuti amafuna moyo wanga?

2 Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate, wanga sacita kanthu kakakuru kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji cinthu cimeneci? Si kutero ai.

3 Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Jonatani asadziwe ici, kuti angamve cisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazilimodzi.

4 Ndipo Jonatani anati kwa Davide, Ciri conse mtima wako unena, ndidzakucitira.

5 Nati Davide kwa Jonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lacitatu madzulo ace.

6 Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pacaka ya banja lao lonse.

7 Tsono akati, Cabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundicitira coipa.

8 Cifukwa cace ucitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamcititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli coipa ciri conse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?

9 Ndipo Jonatani anati, lai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukucitira coipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?

10 Tsono Davide anati kwa Jonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa?

11 Nati Jonatani kwa Davide, Tiyeni timuke kuthengo. Namuka onse awiri kuthengoko.

12 Ndipo Jonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israyeli, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkuca, onani, pakakhala kanthu kabwino kakucitira Davide, sindidzakutumira mthenga ndi kukuululira kodi?

13 Mulungu alange Jonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukucitira coipa, ine osakuululira, ndi kukucotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.

14 Ndipo undionetsere cifundo ca Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe;

15 komanso usaleke kucitira cifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse; mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Da vide pa dziko lapansi.

16 Comweco Jonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.

17 Ndipo Jonatani anamlumbiritsa Davide kaciwiri, cifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.

18 Tsono Jonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.

19 Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mrandu uja, nukhale pa mwala wa Ezeri.

20 Ndipo ine ndidzaponya mibvi itatu pambali pace, monga ngati ndirikuponya pacandamali.

21 Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune mibviyo, Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mibvi iri cakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.

22 Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mibvi iri kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke.

23 Ndipo za cija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.

24 Comweco Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya.

25 Mfumu nikhala pa mpando wace, monga adafocita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Jonatani anaimirira, ndi Abineri anakhala pa mbali ya Sauli; koma Davide anasoweka pamalo pace.

26 Koma Sauli sananena kanthu tsiku lomwelo; cifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.

27 Ndipo kunali tsiku laciwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pace; ndipo Sauli anati kwa Jonatani mwana wace, Mwana wa Jese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?

28 Ndipo Jonatani anayankha Sauli, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu;

29 nati, Ndiloleni, ndimuke; cifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndicoke, ndikaone abale anga. Cifukwa ca ici safika ku gome la mfumu.

Sauli aipidwa ndi Jonatani

30 Pamenepo Sauli anapsa mtima ndi Jonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Jeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?

31 Popeza nthawi yonse mwana wa Jeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Cifukwa cace tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu,

32 Ndipo Jonatani anayankha Sauli atate wace, nanena, Aphedwe cifukwa ninji? anacitanji?

33 Ndipo Sauli anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Jonatani anazindikira kuti atate wace anatsimikiza mtima kupha Davide.

34 Pamenepo Jonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku laciwiri la mwezi, pakuti mtima wace unali ndi cisoni cifukwa ca Davide, popeza atate wace anamcititsa manyazi.

Davide ndi Jonatani alekana

35 Ndipo m'mawa, Jonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnayamata.

36 Ndipo anauza mnyamata waceyo, Thamanga uzikatola mibvi Imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya mubvi kuutumphitsa iye.

37 Ndipo mnyamatayo atafika pa malo a mubvi umene Jonatani anauponya, Jonatani anapfuulira mnyamatayo, nati, Mubviwo suli m'tsogolo mwako kodi?

38 Ndipo Jonatani anapfuulira mnyamatayo, nati, Yendesa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Jonatani anatola mibvi, nafika kwa mbuye wace.

39 Koma mnyamatayo sanadziwa kanthu; Davide ndi Jonatani okha anadziwa za mranduwoo.

40 Ndipo Jonatani anapatsa mnyamata wace zida zace, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumudzi.

41 Pomwepo pocoka mnyamatayo, Davide anauka cakumwera, nagwa nkhope yace pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.

42 Ndipo Jonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yanga ndi mbeu yako, nthawi zamuyaya.

43 Ndipo iye ananyamuka nacoka; koma Jonatani anamuka kumudzi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31