1 Samueli 2 BL92

Coyamikira ca Hana

1 Ndipo Hana anapemphera, natiMtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova,Nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova;Pakamwa panga pakula kwa adani anga;Popeza ndikondwera m'cipulumutsocanu.

2 Palibe wina woyera ngati Yehova;Palibe wina koma Inu nokha;Palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

3 Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero;M'kamwa mwanu musaturuke zolulutsa;Cifukwa Yehova ali Mulungu wanzeru,Ndipo iye ayesa zocita anthu.

4 Mauta a amphamvu anathyoka,Koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m'cuuno.

5 Amene anakhuta anakasuma cakudya;Koma anjalawo anacira;Inde cumba cabala asanu ndi awiri:Ndipo iye amene ali ndi ana ambiri acita liwondewonde.

6 Yehova amapha, napatsa moyo:Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.

7 Yehova asaukitsa, nalemeza;Acepetsa, nakuzanso.

8 Amuutsa waumphawi m'pfumbi,Nanyamula wosowa padzala,Kukamkhalitsa kwa akalonga;Ndi kuti akhale naco colowa ca cimpando ca ulemerero;Cifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova,Ndipo iye anakhazika dziko pa izo,

9 Adzasunga mapazi a okoodedwaace,Koma oipawo adzawakhalitsa cete mumdima;Pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu,

10 Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika;Kumwamba iye adzagunda pa iwo:Yehova adzaweruza malekezero a dziko:Ndipo adzapatsa mphamvu mfumuyace,Nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wace.

11 Ndipo Elikana anauka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo.

Kucimwa kwa ana a Eli

12 Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwa Yehova.

13 Ndipo macitidwe a ansembe akucitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu ali yense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama iri ciwirire, ndi cobvuulira ca ngowe ca mana atatu m'dzanja lace;

14 nacipisa m'cimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene cobvuuliraco cinaiturutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yace. Adafotero ku Silo ndi Aisrayeli onse akufika kumeneko.

15 Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaoce; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi.

16 Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, lai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda.

17 Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikuru ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova.

18 Koma Samueli anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'cuuno ndi efodi wabafuta.

19 Ndiponso amace akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye caka ndi caka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wace kudzapereka nsembe ya pacaka.

20 Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wace, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.

21 Ndipo Yehova anakumbukila Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samueli anakula pamaso pa Yehova.

22 Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ace anacitira Aisrayeli onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la cihema cokomanako.

23 Ndipo iye ananena nao, Mumacitiranji zotere? popeza ndirinkumva za macitidwe anu oipa kwa anthu onsewa.

24 Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndirikuimva siri yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova.

25 Munthu akacimwira munthu mnzace oweruza adzaweruza mrandu wace; koma ngati munthu acimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, cifukwa Yehova adati adzawaononga.

26 Ndipo mwanayo Samueli anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima.

Mneneri aneneratu za kupasuka kwa banja la Eli

27 Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Aigupto, m'nyumba ya Farao?

28 Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israyeli, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, nabvale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israyeli?

29 Nanga umaponnderezeranji nsembe yanga ndi copereka canga, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo ucitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisrayeli, anthu anga?

30 Cifukwa cace Yehova Mulungu wa Israyeli akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Cikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.

31 Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba,

32 Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m'malo mwa zabwino zonse iye akadacitira Israyeli. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba cikhalire.

33 Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha pa guwa langa, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako cisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri.

34 Ndipo ici cimene cidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Pinehasi, cidzakhala cizindikilo kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.

35 Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzacita monga cimene ciri mumtima mwanga ndi m'cifuniro canga; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.

36 Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi cakudya, nadzati, Mundipatsetu nchito yina ya wansembe, kuti ndikaona kakudya.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31