1 Samueli 6 BL92

Afilisti abweza likasa ku dziko la Aisrayeli

1 Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.

2 Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Ticitenji ndi likasa la Yehova? mutidziwitse cimene tilitumize naco kumalo kwace.

3 Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israyeli, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yoparamula, mukatero mudzaciritsidwa, ndi kudziwa cifukwa cace dzanja lace liri pa inu losacoka.

4 Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yoparamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolidi, ndi mbewa zisanu zagolidi, monga mwa ciwerengo ca mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.

5 Cifukwa cace muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo mucitire ulemu Mulungu wa lsrayeli; kuti kapena adzaleza dzanja lace pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu.

6 Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aaigupto ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sana lola anthuwo amuke, iye atacita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?

7 Cifukwa cace tsono, tengani, nimukonze gareta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli cikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagareta, muzicotsere ana ao kunka nao kwanu;

8 ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaretapo; nimuike zokometsera zagolidi, zimene muzipereka kwa iye ngati nsembe yoparamula, m'bokosi pam bali pace; nimulitumize licoke.

9 Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire ace ace ku Betisemesi, iye anaticitira coipa ici cacikuru; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, siliri lace; langotigwera tsokali.

10 Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagareta, natsekera anao kwao;

11 naika likasa la Yehova pagaretapo, ndi bokosi m'mene munali mbewa zagolidi ndi zifanizo za mafundo ao.

12 Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betisemesi, niziyenda mumseu, zirikulira poyenda; sizinapambukira ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betisemesi.

13 Ndipo a ku Betisemesi analikumweta tirigu wao m'cigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwerapakuliona.

14 Ndipo garetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betisemesi, ndi kuima momwemo, pa mwala waukuru; ndipo anawaza matabwa a garetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.

15 Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolidi, naziika pa mwala waukuruwo; ndipo anthu a ku Betisemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.

16 Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekroni tsiku lomwelo.

17 Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolidi amene anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yoparamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekroni limodzi;

18 ndiponso mbewa zagolidi, monga ciwerengo ca midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, midzi ya malinga, ndi midzi ya kumiraga; kufikira ku mwala waukuru, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betisemesi.

19 Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betisemesi, cifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, cifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe akuru.

Likasa lisungidwa ku Kiriati-yearimu

20 Ndipo a ku Betisemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakuticokera ife?

21 Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriati-yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31