1 Samueli 30 BL92

Davide alanditsa a ku Zikilaga m'manja mwa Aamaleki

1 Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ace ku Zikilaga tsiku lacitatu, Aamaleki adaponya nkhondo yobvumbulukira kumwera, ndi ku Zikilaga, nathyola Zikilaga nautentha ndi moto;

2 nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akuru ndi ang'ono; sanapha mmodzi, koma anawatenga, namuka.

3 Ndipo pamene Davide ndi anthu ace anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao amuna ndi akazi anatengedwa ukapolo.

4 Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.

5 Ndipo akazi awiri a Davide anatengedwa ukapolo, Ahinoamu wa ku Jezreeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli.

6 Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi cisoni, yense cifukwa ca ana ace amuna ndi akazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wace.

7 Ndipo Davide ananena ndi Abyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abyatara nabwera ndi efodi kwa Davide.

8 Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Lonriola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.

9 Comweco Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena.

10 Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, cifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.

11 Ndipo ena anapeza M-aigupto kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa cakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;

12 nampatsanso cigamphu ca ncinci ya nkhuyu ndi ncinci ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wace unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya cakudya, osamwa madzi.

13 Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? ufumira kuti? Nati iye, Ndiri mnyamata wa ku Aigupto, kapolo wa M-amaleki; mbuye wanga anandisiya, cifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.

14 Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebi; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilaga ndi moto.

15 Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.

16 Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, cifukwa ca cofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.

17 Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wace; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamila, nathawa.

18 Ndipo Davide analanditsa zonse anazitenga Aamaleki, napulumutsa akazi ace awiri.

19 Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakuru, ana amuna kapena ana akazi, kapena cuma kapena dna ciri conse ca zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse.

20 Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipitikitsa patsogolo pa zoweta zao zao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide.

21 Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anaturuka kucingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji.

22 Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pace a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuka nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wace ndi ana ace, kuti acoke nao namuke.

23 Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe.

24 Ndipo ndani adzabvomerezana nanu mrandu uwu? Pakuti monga gawo lace la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lace la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana cimodzimodzi.

25 Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ici, cikhale lemba ndi ciweruzo pa Aisrayeli.

26 Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilaga, anatumizako za zofunkhazo kwa akuru a Yuda, ndiwo abwenzi ace, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.

27 Anatumiza kwa iwo a ku Beteli, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwela, ndi kwa iwo a ku Yatiri;

28 ndi kwa iwo a ku Aroeri, ndi kwa iwo a ku Sifimoti, ndi kwa iwo a ku Estimoa;

29 ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a m'midzi ya Ayerameli, ndi kwa iwo a m'midzi ya Akeni;

30 ndi kwa iwo a ku Horima, ndi kwa iwo a ku Korasani, ndi kwa iwo a ku Ataki;

31 ndi kwa iwo a ku Hebroni, ndi kumalo konse kumene Davide ndi anthu ace adafoyendayenda.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31