1 Samueli 18 BL92

Ubwenzi wa Davide ndi Jonatani

1 Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Sauli, mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.

2 Ndipo Sauli anamtenga tsiku lomwelo, osamlolanso apite kwao kwa atate wace.

3 Pamenepo Jonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.

4 Ndipo Jonatani anabvula maraya ace anali nao, napatsa Davide, ndi zobvala zace, ngakhale lupanga lace, ndi uta wace, ndi lamba lace.

5 Ndipo Davide anaturuka kunka kuli konse Sauli anamtumako, nakhala wocenjera; ndipo Sauli anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ici cinakomera anthu onse, ndi anyamata a Sauli omwe.

6 Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu akazi anaturuka m'midzi yonse ya Israyeli, ndi kuyimba ndi kubvina, kuti akakomane ndi mfumu Sauli, ndi malingaka, ndi cimwemwe, ndi zoyimbira.

7 Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuyimba kwao, nati,Sauli anapha zikwi zace,Koma Davide zikwi zace zankhani.

Sauli aipidwa ndi Davide

8 Koma Sauli anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawereogera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; cimperewera ncianioso, koma ufumu wokha?

9 Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m'tsogolo mwace, Sauli anakhala maso pa Davide.

10 Ndipo kunali m'mawa mwace, mzimu woipa wocokera kwa Mulungu unamgwira Sauli mwamphamvu, iye nalankhula moyaruka m'nyumba yace; koma Davide anayimba ndi dzanja lace, monga amacita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Sauli munali mkondo.

11 Ndipo Sauli anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kucoka pamaso pace.

12 Ndipo Sauli anaopa Davide, cifukwa Yehova anali naye, koma adamcokera Sauli.

13 Cifukwa cace Sauli anamcotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wace wa anthu cikwi cimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kuturuka ndi kubwera nao.

14 Ndipo Davide anakhala wocenjera m'mayendedwe ace onse; ndipo Yehova anali naye.

15 Ndipo pamene Sauli anaona kuti analikukhala wocenjera ndithu anamuopa.

16 Koma Aisrayeli onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kuturuka ndi kulowa nao.

Davide mkamwini wa Sauli

17 Ndipo Sauli anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkuru, dzina lace Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Sauli anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.

18 Ndipo Davide anati kwa Sauli, Ine ndine yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga liri lotani m'Israyeli, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?

19 Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Sauli kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adrieli Mholati kukhala mkazi wace.

20 Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli anakonda Davide; ndipo pakumva Sauli, anakondwera nako.

21 Nati Sauli, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Cifukwa cace Sauli ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kaciwiri.

22 Ndipo Sauli analamulira anyamata ace, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ace onse akukondani; cifukwa cace tsono, khalani mkamwini wa mfumu.

23 Ndipo anyamata a Sauli analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muciyesera cinthu copepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndiri munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.

24 Ndipo anyamata a Sauli anamuuza, kuti, Anatero Davide.

25 Nati Sauli, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna colowolera cina, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere cilango adani a mfumu. Koma Sauli anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.

26 Ndipo pamene anyamata ace anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu.

27 Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ace, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Sauli anampatsa Mikala mwana wace wamkazi akhale mkazi wace.

28 Ndipo Sauli anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Sauli anamkonda Davide.

29 Sauli nayamba kumuopa Davide kopambana; ndi Sauli anali mdani wa Davide masiku onse.

30 Pomwepo mafumu a Afilisti anaturuka; ndipo nthawi zonse anaturuka iwo, Davide anali wocenjera koposa anyamata onse a Sauli, comweco dzina lace linatamidwa kwambiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31