1 Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisrayeli anamanga ku citsime ca m'Jezreeli.
2 Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ace ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi.
3 Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa acitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Sauli, mfumu ya Israyeli, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.
4 Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwace kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yace? Si ndi mitu ya anthu awa?
5 Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti,Sauli anapha zikwi zace,Koma Davide zikwi zace zankhani?
6 Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kuturuka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona coipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.
7 Cifukwa cace, bwerera, numuke mumtendere, kuti angaipidwe mtima nawe akalonga a Afilisti.
8 Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinacitanji? Ndipo munapeza ciani mu mnyamata wanu nthawi yonse ndiri pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?
9 Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, iye asamuke nafe kunkhondoko.
10 Cifukwa cace ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutaca.
11 Comweco Davide analawirira, iye ndi anthu ace, kuti amuke m'mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera ku Jezreeli.