1 Samueli 17 BL92

Davide apha Goliati

1 Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-damimu.

2 Ndipo Sauli ndi anthu a Israyeli anasonkhana, namanga zithando pa cigwa ca Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti.

3 Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisrayeli anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali cigwa.

4 Ndipo ku zithando za Afilisti kunaturuka ciwinda, dzina lace Goliate wa ku Gati, kutalika kwace ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi cikhato.

5 Ndipo anali ndi cisoti camkuwa pamutu pace, nabvala maraya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa,

6 nakuta msongolo wace ndi cobvala camkuwa, ndiponso pacikota pace panali nthungo yamkuwa.

7 Ndipo mtengo wa mkondo wace unali ngati mtanda woombera nsaru; ndi khali la mkondowo linalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a citsulo; ndipo womnyamulira cikopa anamtsogolera.

8 Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israyeli, nanena nao, Munaturukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Sauli? mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.

9 Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikamlaka, ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife.

10 Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israyeli lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri.

11 Ndipo pamene Sauli ndi Aisrayeli onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.

12 Tsono Davide anali mwana wa M-efrati uja wa ku Betelehemu-Yuda, dzina lace ndiye Jese; ameneyu anali nao ana amuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Sauli munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.

13 Ndipo ana atatu akuru a Jese anatsata Sauli kunkhondoko; ndi maina ao a ana ace atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliabu woyambayo, ndi mnzace womponda pamutu pace Abinadabu, ndi wacitatu Sama.

14 Ndipo Davide anali wotsiriza; ndi akuru atatuwo anamtsata Sauli.

15 Koma Davide akamuka kwa Sauli, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wace ku Betelehemu.

16 Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai.

17 Ndipo Jese anati kwa Davide mwana wace, Uwatengere abale ako efa watirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;

18 nunyamule ncinci izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa cikwi cao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire cikole cao,

19 Tsono Sauli, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israyeli, anali m'cigwa ca Ela, ku nkhondo ya Afilisti.

20 Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Jese; ndipo iye anafika ku linga la magareta, napeza khamu lirikuturuka kunka poponyanira nkhondo lirikupfuula.

21 Ndipo Israyeli ndi Afilisti anandandalitsa nkhondo zao, khamu tina kuyang'anana ndi khamu lina.

22 Ndipo Davide anasiya akatundu ace m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nalankhula abale ace.

23 Ndipo m'mene iye anali cilankhulire nao, onani cinakwerako ciwindaco, Mfilisti wa ku Gati, dzina lace ndiye Goliate, woturuka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.

24 Ndipo Aisrayeli onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri.

25 Nati Aisrayeli, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israyeli, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi cuma cambiri, nidzampatsa mwana wace wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wace yaufulu m'Israyeli.

26 Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamcitira ciani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kucotsa tonzo lace pakati pa Israyeli? pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?

27 Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamcitira munthu wakumupha iye mwakuti mwakuti.

28 Ndipo Eliabu mkuru wace anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'cipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.

29 Ndipo Davide anati, Ndacitanji tsopano? Palibe cifukwa kodi?

30 Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo.

31 Ndipo pamene mau adanena Davide anamveka, anawapitiriza kwa Sauli; ndipo iye anamuitana.

32 Ndipo Davide anati kwa Sauli, Asade nkhawa munthu ali yense cifukwa ca iyeyo; ine kapolo wanu ndidzapita kuponyana ndi Mfilisti uyu.

33 Ndipo Sauli anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wace.

34 Ndipo Davide anati kwa Sauli, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina cimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo,

35 ndinacithamangira, ndi kucikantha, ndi kuiturutsa m'kamwa mwace; ndipo pamene cinaneliukira, ndinagwira cowa lace ndi kucikantha ndi kucipha.

36 Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi cimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.

37 Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya cimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu, Ndipo Sauli anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.

38 Ndipo Sauli anabveka Davide zobvala zace za iye yekha, nambveka cisoti camkuwa pamutu pace, nambvekanso maraya aunyolo.

39 Ndipo Davide anamanga lupanga lace pamwamba pa zobvala zace, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazibvula Davide.

40 Natenga ndodo yace m'dzanja lace nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo cibete; ndi coponyera miyala cinali m'dzanja lace, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.

41 Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula cikopa cace anamtsogolera.

42 Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata cabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.

43 Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine garu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide nachula milungu yace.

44 Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za kuthengo.

45 Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza.

46 Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukucotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu.

47 Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo iye adzakuperekani inu m'manja athu.

48 Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.

49 Ndipo Davide anapisa dzanja lace m'thumba mwace, naturutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi cafufumimba.

50 Comweco Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa coponyera cace, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.

51 Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lace, nalisolola m'cimace, namtsiriza nadula nalo mutu wace. Ndipo pakuona Afilisti kuti ciwinda cao cidafa, anathawa.

52 Ndipo anthu a Israyeli ndi Ayuda ananyamuka, napfuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kucigwako, ndi ku zipata za Ekroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saraimu, kufikira ku Gad ndi ku Ekroni.

53 Ndipo ana a Israyeli atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao.

54 Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zace anazisunga m'hema wace.

55 Ndipo pamene Sauli anaona Davide alikuturukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abineri, kazembe wa khamu la nkhondo, Abineri, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abineri, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.

56 Ndipo mfumu inati, Ufunsire kuti mnyamatayo ndi mwana wa yani.

57 Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abineri anamtenga, nafika naye pamaso pa Sauli, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lace.

58 Ndipo Sauli anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndiri mwana wa kapolo wanu Jese wa ku Betelehemu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31