1 Samueli 15 BL92

Sauli alamulidwa aononge Amaleki

1 Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ace Aisrayeli; cifukwa cace tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova.

2 Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera cimene Amaleki anacitira Israyeli, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kuturuka m'Aigupto.

3 Muka tsopano, nukanthe Amaleki, nuononge konse konse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamila ndi buru.

4 Ndipo Sauli anamemeza anthu, nawawerenga ku Telayimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.

5 Ndipo Sauli anafika ku mudzi wa Amaleki, nalalira kucigwa.

6 Ndipo Sauli anauza Akeni kuti, Mukani, cokani mutsike kuturuka pakati pa Aamaleki, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munacitira ana a Israyeli onse zabwino, pakufuma iwo ku Aigupto. Comwece Akeni anacoka pakati pa Aamaleki.

7 Ndipo Sauli anakantha Aamaleki, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri; ciri pandunji pa Aigupto.

8 Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleki, naononga konse konse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.

9 Koma Sauli ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi ana a nkhosa, ndi zabwino zonse, sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konse konse.

Samueli adzudzula Sauli pa kusamvera kwace

10 Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samueli, nati,

11 Kundicititsa cisoni kuti ndinaika Sauli akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanacita malamulo anga, Ndipo Samueli anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.

12 Ndipo Samueli analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Sauli; ndipo munthu anamuuza Samueli kuti, Sauli anafika ku Karimeli, ndipo taonani, anaimika cikumbutso cace, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.

13 Ndipo Samueli anadza kwa Sauli; ndipo Sauli anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinacita lamulo la Yehova.

14 Ndipo Samueli anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndirikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndirikumva, nciani?

15 Ndipo Sauli anati, Anazitenga kwa Aamaleki; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konse konse.

16 Pomwepo Samueli ananena ndi Sauli, Imani, ndidzakudziwitsani cimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

17 Nati Samueli, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israyeli? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israyeli,

18 Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konse konse Aamaleki akucita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.

19 Cifukwa ninji tsono simunamvera mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova?

20 Ndipo Sauli ananena ndi Samueli, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleki, ndi Aamaleki ndinawaononga konse konse.

21 Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng'ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.

22 Ndipo Samueli anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kuchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo,

23 Pakuti kupanduka kuli ngati coipa ca kucita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yacabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

24 Ndipo Sauli anati kwa Samueli, Ndinacimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; cifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.

25 Cifukwa cace tsono, mukhululukire cimo langa, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova.

26 Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israyeli.

27 Ndipo pakupotoloka Samueli kuti acoke, iye anagwira cilezi ca mwinjiro wace, ndipo cinang'ambika.

28 Ndipo Samueli ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israyeli lero kuucotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.

29 Ndiponso Wamphamvu wa Israyeli sanama kapena kulapa; popeza iye sali munthu kuti akalapa.

30 Pomwepo iye anati, Ndinacimwa, koma mundicitire ulemu tsopano pamaso pa akuru a anthu anga, ndi pamaso pa Israyeli, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.

31 Comweco Samueli anabwerera natsata Sauli; ndi Sauli analambira Yehova.

32 Ndipo Samueli anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleki. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.

33 Ndipo Samueli anati, Monga lupanga lako linacititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samueli anamdula Agagi nthuli nthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.

34 Pamenepo Samueli ananka ku Rama; ndi Sauli anakwera kunka ku nyumba yace ku Gibeya wa Sauli.

35 Ndipo Samueli sanadzanso kudzaona Sauli kufikira tsiku la imfa yace; koma Samueli analira cifukwa ca Sauli; ndipo Yehova anali ndi cisoni kuti anamlonga Sauli mfumu ya Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31