1 Samueli 23 BL92

Davide alanditsa a ku Keila

1 Tsono anauza Davide, kuti, Onani Afilisti alikuponyana ndi Keila, nafunkha za m'madwale.

2 Cifukwa cace Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila.

3 Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Taonani, ife tikhalira m'mantha ku Yuda kuno; koposa kotani nanga tikafika ku Keila kuponyana ndi makamu a nkhondo a Afilisti.

4 Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.

5 Comweco Davide ndi anthu ace anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.

6 Ndipo kunali kuti Abyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lace.

7 Ndipo anthu anauza Sauli kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Sauli anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.

8 Ndipo Sauli anamemeza anthu onse kunkhondo, kuti atsikire ku Keila, kumangira misasa Davide ndi anthu ace.

9 Ndipo Davide anadziwa kuti Sauli analikulingalira zomcitira zoipa; nati kwa Abyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.

10 Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israyeli, mnyamata wanu wamva zoona kuti Sauli afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo cifukwa ca ine.

11 Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lace? Kodi Sauli adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israyeli, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika.

12 Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Sauli? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.

13 Potero Davide ndi anyamata ace, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, naturuka ku Keila, nayendayenda kuli konse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Sauli kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata.

Davide ndi Jonatani abwereza kupangana

14 Ndipo Davide anakhala m'cipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'cipululu ca Zifi. Ndipo Sauli anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereka m'dzanja lace.

15 Ndipo Davide anaona kuti Sauli adaturuka kudzafuna moyo wace; Davide nakhala m'cipululu ca Ziti m'nkhalango.

16 Ndipo Jonatani mwana wa Sauli ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lace mwa Mulungu.

17 Ndipo iye ananena naye, Usaopa; cifukwa dzanja la Sauli atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israyeli, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, icinso Sauli atate wanga acidziwa.

18 Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Jonatani anapita ku nyumba yace.

19 Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Sauli ku Gibeya, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango, m'phiri la Hakila. Umene Uri kumwera kwa cipululu?

20 Cifukwa cace mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu.

21 Sauli nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; cifukwa munandicitira ine cifundo.

22 Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; cifukwa anandiuza kuti iye acita mocenjera ndithu.

23 Cifukwa cace yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.

24 Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Sauli; koma Davide ndi anthu ace anali ku cipululu ca Maoni, m'cigwa ca kumwera kwa cipululu.

25 Ndipo Sauli ndi anthu ace anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; cifukwa cace anatsikira kuthanthweko, nakhala m'cipululu ca Maoni. Ndipo pamene Sauli anamva ici, iye anamlondola Davide m'cipululu ca Maoni.

26 Ndipo Sauli anamuka mbali yina ya phiri, Davide ndi anthu ace kutseri kwace; ndipo Davide anafulumira kuthawa, cifukwa ca kuopa Sauli; popeza Sauli ndi anthu ace anazinga Davide ndi anthu ace kwete kuti awagwire.

27 Koma mthenga unafika kwa Sauli ndi kuti, Mufulumire kubwerera; popeza nkhondo yobvumbulukira ya Afilisti yalowa m'dziko.

28 Comweco Sauli anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; cifukwa cace anachula dzina lace la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.

29 Ndipo Davide anakwera kucokera kumeneko, nakhalam'ngaka za Engedi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31