1 Samueli 31 BL92

Sauli ndi ana ace atatu aphedwa ndi Afilisti pa Giliboa

1 Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisrayeli; Aisrayeli nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Giliboa.

2 Ndipo Afilisti anapitikitsa, osawaleka Sauli ndi ana ace; ndipo Afilisti anapha Jonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisua, ana a Sauli.

3 Ndipo nkhondoyo inamkulira Sauli kwambiri, oponya mibvi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukuru cifukwa ca oponya mibviyo.

4 Tsono Sauli ananena ndi wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka, Koma woo nyamula zida zace anakana; cifukwa anaopa ndithu. Cifukwa cace Sauli anatenga lupanga lace naligwera.

5 Ndipo pakuona kuti Sauli anafa, wonyamula zida zace yemwe, anagwera lupanga lace, nafera limodzi ndi iye.

6 Comweco adamwalira pamodzi Sauli ndi ana ace atatu, ndi wonyamula zida zace, ndi anthu ace onse, tsiku lomwe lija.

7 Ndipo pamene Aisrayeli akukhala tsidya lina la cigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordano, anaona kuti Aisrayeli alikuthawa, ndi kuti Sauli ndi ana ace anafa, iwowa anasiya midzi yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.

8 Ndipo kunali m'mawa mwace, pakubwera Afilisti kubvula akufawo, anapeza Sauli ndi ana ace atatu ali akufa m'phiri la Giliboa.

9 Ndipo anadula mutu wace, natenga zida zace, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira ku nyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu.

10 Ndipo anaika zida zace m'nyumba ya Asitarote; napacika mtembo wace ku linga la ku Betisani.

11 Koma pamene a ku Jabezi Gileadi anamva zimene Afilisti anamcitira Sauli,

12 ngwazi zonse zinanyamuka ndi kucezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Sauli, ndi mitembo ya ana ace, pa linga la Betisani; nafika ku Jabezi Gileadi naitentha kumeneko.

13 Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo uli m'Jabezi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31