1 Samueli 9 BL92

Sauli afuna aburu olowerera a atate wace

1 Ndipo panali munthu Mbenlamlni, dzina lace ndiye Kisi, mwana wa Abiyeli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.

2 Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lace Sauli, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israyeli panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu onse ena anamlekeza m'cifuwa.

3 Ndipo aburu a Kisi, atate wa Sauli, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Sauli mwana wace, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna aburuwo.

4 Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efraimu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeza; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu; koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.

5 Pamene anafika ku dziko la Zufi, Sauli anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira aburuwo, ndi kutenga nkhawa cifukwa ca ife.

6 Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amcitira ulemu; zonse azinena zicitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tirikuyendera.

7 Ndipo Sauli ananena ndi mnyamata wace, Koma taona, tikapitako nmtengere ciani munthuyo? popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tiribe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tiri naco ciani?

8 Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Sauli nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.

9 Kale m'Israyeli, munthu akati afunse kwa Mulungu, adafotero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wochedwa mneneri makono ano, anachedwa mlauli kale.

10 Pamenepo Sauli anati kwa mnyamata wace, Wanena bwino; tiye tipite. Comweco iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.

11 Pakukwera kumudziko anapeza anthu akazi alikuturuka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?

12 Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;

13 mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Cifukwa cace kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza.

14 Ndipo iwowa anakwera kumudzi; ndipo m'mene analowa m'mudzimo, onani, Samueli anaturukira pali Iwo, kuti akakwere kumsanje.

Sauli akomana ndi Samueli

15 Ndipo Yehova anaululiratu m'khutu la Samueli dzulo lace la tsiku limene Sauli anabwera, kuti,

16 Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wocokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

17 Ndipo pamene Samueli anaona Sauli, Yehova anati kwa iye, Ona munthu amene ndinakuuza za iye! ameneyu adzaweruza anthu anga.

18 Pomwepo Sauli anayandikira kwa Samueli pakati pa cipata, nati, Mundidziwitse nyumba ya mlauliyo iri kuti.

19 Ndipo Samueli anayankha Sauli nati, Inendinemlauliyo. Kwera, batsogola kumsanje, pakuti mudzadya ndi ine lero; ndipo m'mawa ndidzakulola upite, ndi kukudziwitsa zonse ziri mumtima mwako.

20 Za aburu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo cifuniro conse ca Israyeli ciri kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako?

21 Ndipo Sauli anayankha nati, Sindiri Mbenjamini kodi, wa pfuko laling'ono mwa Israyeli? Ndiponso banja lathu nlocepa pakati pa mabanja onse a pfuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?

22 Ndipo Samueli anatenga Sauli ndi mnyamata wace, napita nao ku cipinda ca alendo, nawakhalitsa pa malo a ulemu pakati pa oitanidwa onse; ndiwo anthu monga makumi atatu.

23 Ndipo Samueli ananena ndi wophika, Tenga nyama ndinakupatsa, ndi kuti, Ibakhala ndi iwe.

24 Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wace, nauika pamaso pa Sauli. Ndipo Samueli anati, Onani cimene tinakuikirani muciike pamaso panu, nudye; pakuti ici anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwoo Comweco Sauli anadya ndi Samueli tsiku lija.

25 Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumudzi, iye anakamba ndi Sauli pamwamba pa nyumba yace.

26 Ndipo anauka mamawa; ndipo kutaca, Samueli anaitana Sauli ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Sauli anauka, naturuka onse awiri, iye ndi Samueli, kunka kunja.

27 Ndipo pamene analikutsika polekeza mudzi, Samueli ananena ndi Sauli, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29 30 31