22 Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mibvi iri kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke.
23 Ndipo za cija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.
24 Comweco Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya.
25 Mfumu nikhala pa mpando wace, monga adafocita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Jonatani anaimirira, ndi Abineri anakhala pa mbali ya Sauli; koma Davide anasoweka pamalo pace.
26 Koma Sauli sananena kanthu tsiku lomwelo; cifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.
27 Ndipo kunali tsiku laciwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pace; ndipo Sauli anati kwa Jonatani mwana wace, Mwana wa Jese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?
28 Ndipo Jonatani anayankha Sauli, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu;