22 Nati kwa iye wosunga nyumba ya zobvala, Turutsira otumikira Baala onse zobvala. Nawaturutsira zobvala.
23 Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.
24 Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndirikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wace kulipa moyo wace.
25 Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asaturuke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka ku mudzi wa nyumba ya Baala.
26 Naturutsa zoimiritsa zija zinali m'nyumba ya Baala, nazitentha.
27 Nagamula fane la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.
28 Momwemo Yehu anaononga Baala m'Israyeli.