13 Koma sanapangira nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera ziri zonse zagolidi, kapena zotengera ziri zonse zasiliva, kuzipanga ndi ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Yehova;
14 pakuti anazipereka kwa iwo akugwira nchitoyi, nakonza nazo nyumba ya Yehova.
15 Ndipo sanawerengera anthu, amene anapereka ndaramazi m'manja mwao kuti apatse ogwira nchito; popeza anacita mokhulupirika.
16 Ndarama za nsembe zoparamula ndi ndarama za nsembe yaucimo sanabwera nazo ku nyumba ya Yehova; nza ansembe izi.
17 Pamenepo Hazaeli mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yace kukwera ku Yerusalemu.
18 Koma Yoasi mfumu ya Yuda: anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yoramu, ndi Ahaziya, makolo ace, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zace zace, ndi golidi yense anampeza pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Aramu; motero anabwerera kucoka ku Yerusalemu.
19 Macitidwe ena tsono a Yoasi ndi zonse adazicita sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?