7 Pamenepo mfumu Yoasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndarama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.
8 Nabvomera ansembe kusalandiranso ndarama za anthu, kapena kukonza mogamuka nvumba.
9 Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola ciboo pa cibvundikilo cace, naliika pafupi pa guwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndarama zonse anabwera nazo anthu ku nyumba ya Yehova,
10 Ndipo pakuona kuti ndarama zidacuruka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkuru wansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.
11 Napereka ndarama zoyesedwa m'manja mwa iwo akucita nchitoyi, akuyang'anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira nchito ya pa nyumba ya Yehova,
12 ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.
13 Koma sanapangira nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera ziri zonse zagolidi, kapena zotengera ziri zonse zasiliva, kuzipanga ndi ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Yehova;