6 Komatu sanalekana nazo zolakwa za nyumba ya Yerobiamu, zimene analakwitsa nazo Israyeli, nayenda m'mwemo; nicitsalanso cifanizo m'Samariya.
7 Koma mfumu ya Aramu sanasiyira Yoahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magareta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati pfumbi lopondapo.
8 Macitidwe ena tsono a Yoahazi, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?
9 Ndipo Yoahazi anagona ndi makolo ace, namuika m'Samariya; nakhala mfumu m'malo mwace Yoasi mwana wace.
10 Caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca Yoasi mfumu ya Yuda, Yoasi mwana wa Yoahazi analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi.
11 Nacita coipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli, koma anayendamo.
12 Macitidwe ena tsono a Yoasi, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace yocita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?